Koma ndiribe ine kanthu koti ndinenetse za iye kakulembera kwa mbuye wanga. Cifukwa cace ndamturutsira kwa inu, ndipo makamaka kwa inu, Mfumu Agripa, kuti, ndikatha kumfunsafunsa, ndikhale nako kanthu kakulembera.