Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 23:9-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo cidauka cipolowe cacikuru; ndipo alembi ena a kwa Afarisi anaimirira, natsutsana, nanena, Sitipeza coipa ciri conse mwa munthuyu; ndipo nanga bwanji ngati mzimu kapena mngelo: walankhula naye?

10. Ndipo pamene padauka cipolowe cacikuru, kapitao wamkuru anaopa kuti angamkadzule Paulo, ndipo analamulira asilikari atsike, namkwatule pakati pao, nadze naye kulowa naye m'linga,

11. Ndipo usiku wace Ambuye anaimirira pa iye, nati, Limbika mtima; pakuti monga wandicitira umboni ku Yerusalemu, koteronso uyenera kundicitira umboni ku Roma.

12. Ndipo kutaca, Ayuda anapangana ciwembu, nadzitemberera, ndi kunena kuti sadzadya kapena kumwa kanthu, kufikira atamupha Paulo;

13. ndipo iwo amene adacita cilumbiro ici anali oposa makumi anai.

14. Amenewo anadza kwa ansembe akulu ndi akulu, nati, Tadzitemberera nalo temberero kuti sitidzalawa kanthu kufikira titamupha Paulo.

15. Potero tsopano inu ndi bwalo la akuru muzindikiritse kapitao wamkuru kuti atsikenaye kwa inu, monga ngati mufuna kudziwitsitsa bwino za iye; koma tadzikonzeratu timuphe asanayandikire iye.

16. Koma mwana wa mlongo wace wa Paulo anamva za cifwamba cao, ndipo anadza nalowa m'linga, namfotokozera Paulo.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 23