Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 23:15-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Potero tsopano inu ndi bwalo la akuru muzindikiritse kapitao wamkuru kuti atsikenaye kwa inu, monga ngati mufuna kudziwitsitsa bwino za iye; koma tadzikonzeratu timuphe asanayandikire iye.

16. Koma mwana wa mlongo wace wa Paulo anamva za cifwamba cao, ndipo anadza nalowa m'linga, namfotokozera Paulo.

17. Ndipo Paulo anadziitanira kenturiyo wina, nati, Pita naye mnyamata uyu kwa kapitao wamkuru; pakuti ali nako kanthu kakumfotokozera iye.

18. Pamenepo ndipo anamtenga, napita naye kwa kapitao wamkuru, nati, Wam'nsingayo Paulo anandiitana, nandipempha ndidze naye mnyamata uyu kwa inu, ali nako kanthu kakulankhula ndi inu.

19. Ndipo kapitao wamkuru anamgwira dzanja, napita naye padera, namfunsa m'tseri, Ciani ici uli naco kundifotokozera?

20. Ndipo anati, Ayuda anapangana kuti akufunseni mutsike naye Paulo mawa ku bwalo la mirandu, monga ngati mufuna kufunsitsa za iye.

21. Pamenepo musakopedwe nao; pakuti amlalira iye oposa makumi anai a iwo amene anadzitemberera okha kud sadzadya kapena kumwa kufikira atamupha iye; ndipo akonzekeratu tsopano nayang'anira lonjezano lanu.

22. Pamenepo ndipo kapitao wamkuru anauza mnyamatayo apite, namlamulira kuti, Usauze munthu yense kuti wandizindikiritsa izi.

23. Ndipo anaitana akenturiyo awiri, nati, Mukonzeretu asilikari mazana awiri, apite kufikira Kaisareya, ndi apakavalo makumi asanu ndi awiri, ndi anthungo mazana awiri, acoke ora lacitatu la usiku;

24. ndiponso mukonzeretu nyama zobereka amkwezepo Paulo, nampereke wosungika kwa Felike kazembeyo.

25. Ndipo analembera kalata wakuti:

26. Klaudiyo Lusiya kwa kazembe womveketsa Felike, ndikulankhulani.

27. Munthu uyu anagwiridwa ndi Ayuda, ndipo akadaphedwa ndi iwo; pamenepo ndinafikako ine ndi asilikari, ndipo ndinamlanditsa pakumva kuti ndiye Mroma.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 23