Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 23:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Paulo, popenyetsetsa a m'bwalo la akuru anati, Amuna, abale, ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi cikumbu mtima cokoma conse kufikira lero lomwe.

2. Ndipo mkulu wa ansembe Hananiya analamulira akuimirirako ampande pakamwa pace.

3. Pamenepo Paulo anati kwa iye, Mulungu adzakupanda iwe, khoma loyeretsedwa iwe; ndipo kodi ukhala iwe wakundiweruza mlandu monga mwa cilamulo, ndipo ulamulira andipande ine posanga cilamulo?

4. Ndipo iwo akuimirirako anati, Ulalatira kodi mkulu wa ansembe wa Mulungu?

5. Ndipo Paulo anati, Sindinadziwa, abale, kuti ndiye mkulu wa ansembe; pakuti kwalembedwa, Usamnenera coipa mkulu wa anthu ako.

6. Koma pozindikira Paulo kuti ena ndi Asaduki, ndi ena Afarisi, anapfuula m'bwalomo, Amuna, abale, ine ndine Mfarisi, mwana wa Afarisi: andinenera mlandu wa ciyembekezo ndi kuuka kwa akufa.

7. Ndipo pamene adatero, kunakhala cilekano pakati pa Afarisi ndi Asaduki; ndipo osonkhanawo anagawikana.

8. Pakutitu Asaduki anena kuti kulibe kuuka kwa akufa, kapena mngelo, kapena mzimu; koma Afarisi abvomereza ponse pawiri.

9. Ndipo cidauka cipolowe cacikuru; ndipo alembi ena a kwa Afarisi anaimirira, natsutsana, nanena, Sitipeza coipa ciri conse mwa munthuyu; ndipo nanga bwanji ngati mzimu kapena mngelo: walankhula naye?

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 23