Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 21:23-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Cifukwa cace ucite ici tikuuza iwe; tiri nao amuna anai amene anawinda;

24. amenewa uwatenge nudziyeretse nao pamodzi, nuwalipirire, kati amete mutu; ndipo adzadziwa onse kuti zomveka za iwe nzacabe, koma kuti iwe wekhaoso uyenda molunjika, nusunga cilamulo.

25. Kama kunena za amitundu adakhulupirawo, tinalembera ndi kulamulira kuti asale zoperekedwa kwa mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama.

26. Pamenepo Paulo anatenga anthuwo, ndipo m'mawa mwace m'mene anadziyeretsa nao pamodzi, analowa m'Kacisi, nauza cimarizidwe ca masiku a kuyeretsa, kufikira adawaperekera iwo onse mtulo.

27. Ndipo pamene masiku asanu, ndi awiri anati amarizidwe, Ayuda a ku Asiya pomuona iye m'Kacisi, anautsa khamu lonse la anthu, namgwira,

28. napfuula, Amuna a Israyeli, tithandizeni; ameneyu ndi munthu uja anaphunzitsa onse ponsepo ponenera anthu, ndi cilamulo, ndi malo ano; ndiponso anatenga Ahelene nalowa nao m'Kacisi, nadetsa malo ana oyera.

29. Pakuti adaona Trofimo wa ku Efeso kale pamodzi ndi iye mumzinda; ameneyo anayesa kuti Paulo anamtenga nalowa naye kuKacisi.

30. Ndipo mudzi wonse unasokonezeka, ndipo anthu anathamangira pamodzi; nagwira Paulo namkoka kumturutsa m'Kacisi; ndipo pomwepo pamakomo panatsekedwa.

31. Ndipo m'mene anafuna kumupha iye, wina anamuuza kapitao wamkuru wa gululo kuti m'Yerusalemumonse muli pinngu-piringu,

32. Ndipo posacedwa iye anatenga asilikari ndi akenturiyo, nathamanga, nawatsikira; ndipo iwowa, pakuona kapitao wamkuru ndi asilikari, analeka kumpanda Paulo.

33. Pamenepo poyandikira kapitao wamkuru anamgwira iye, nalamulira ammange ndi maunyolo awir; ndipo anafunsira, ndiye yani, ndipo anacita ciani?

34. Koma wina anapfuula kena, wina kena, m'khamumo; ndipo m'mene sanathe kudziwa zoona cifukwa ca phokosolo analamulira amuke naye kulinga.

35. Ndipo pamene anafika pamakwerero, kudatero kuti anamsenza asilikari cifukwa ca kulimbalimba kwa khamulo;

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 21