Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 19:25-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. amenewo iye anawasonkhanitsa pamodzi ndi amisiri a nchito yomweyo, nati, Amuna inu, mudziwa kuti ndi malonda awa ife tipeza cuma cathu.

26. Ndipo muona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, Si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja:

27. ndipo tiopa ife kuti nchito yathuyi idzayamba kunyonyosoka; komanso kuti kacisi wa mlungu wamkazi Artemi adzayamba kuyesedwa wacabe; ndiponso kuti iye adzayamba kutsitsidwa ku ukulu wace, iye amene a m'Asiya onse, ndi onse a m'dziko lokhalamo anthu, ampembedza.

28. Ndipo pamene anamva, anadzala ndi mkwiyo, napfuula, nati, Wamkuru ndi Artemi wa ku Efeso,

29. Ndipo m'mudzi monse munacita piringu-piringu, nathamangira onse pamodzi ku bwalo losewera, atagwira Gayo ndi Aristarko, anthu a ku Makedoniya, alendo anzace a Paulo.

30. Ndipo pamene Paulo anafuna kulowa kwa anthu, akuphunzira ace sanamloleza.

31. Ndipo akulu ena a Asiyanso, popeza anali abwenzi ace, anatumiza mau kwa iye, nampempha asadziponye ku bwalo lakusewera.

32. Ndipo ena anapfuula kanthu kena, ena kanthu kena; pakuti msonkhanowo unasokonezeka; ndipo unyinji sunadziwa cifukwa cace ca kusonkhana.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 19