Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 19:24-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Pakuti munthu wina dzina lace Demetriyo wosula siliva, amene anapanga tiakacisi tasiliva ta Artemi, anaonetsera amisiri phindu lambiri;

25. amenewo iye anawasonkhanitsa pamodzi ndi amisiri a nchito yomweyo, nati, Amuna inu, mudziwa kuti ndi malonda awa ife tipeza cuma cathu.

26. Ndipo muona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, Si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja:

27. ndipo tiopa ife kuti nchito yathuyi idzayamba kunyonyosoka; komanso kuti kacisi wa mlungu wamkazi Artemi adzayamba kuyesedwa wacabe; ndiponso kuti iye adzayamba kutsitsidwa ku ukulu wace, iye amene a m'Asiya onse, ndi onse a m'dziko lokhalamo anthu, ampembedza.

28. Ndipo pamene anamva, anadzala ndi mkwiyo, napfuula, nati, Wamkuru ndi Artemi wa ku Efeso,

29. Ndipo m'mudzi monse munacita piringu-piringu, nathamangira onse pamodzi ku bwalo losewera, atagwira Gayo ndi Aristarko, anthu a ku Makedoniya, alendo anzace a Paulo.

30. Ndipo pamene Paulo anafuna kulowa kwa anthu, akuphunzira ace sanamloleza.

31. Ndipo akulu ena a Asiyanso, popeza anali abwenzi ace, anatumiza mau kwa iye, nampempha asadziponye ku bwalo lakusewera.

32. Ndipo ena anapfuula kanthu kena, ena kanthu kena; pakuti msonkhanowo unasokonezeka; ndipo unyinji sunadziwa cifukwa cace ca kusonkhana.

33. Ndipo anaturutsa Alesandro m'khamumo, kumturutsa iye Ayuda. Ndipo Alesandro anatambasula dzanja, nafuna kudzikanira kwa anthu adasonkhanawo.

34. Koma pozindikira kuti ali Myuda, kunali mau amodzi a kwa onse akupfuula monga maora awiri, Wamkuru ndi Artemi wa Aefeso.

35. Ndipo pamene mlembi adatontholetsa khamulo, anati, Amuna a Efeso inu, munthuyu ndani wosadziwa kuti mudzi wa Aefeso ndiwo wosungira kacisi wa Artemi wamkuru, ndi fano Iidacokera kwa Zeu?

36. Popeza tsono izi sizikanika, muyenera inu kukhala cete, ndi kusacita kanthu kaliuma.

37. Pakuti mwatenga anthu awa, osakhala olanda za m'kacisi, kapena ocitira mulungu wathu mwano.

38. Ngati tsono Demetriyo ndi amisiri okhala naye, ali ndi mlandu ndi munthu, mabwalo a mirandu alipo, ndi ziwanga ziripo; anenezane.

39. Koma ngati mufuna kanthu ka zinthu zina, kadzakonzeka m'msonkhano wolamulidwa.

40. Pakutinso palipo potiopsya kuti adzatineneza za cipolowe ca lero; popeza palibe cifukwa ca kufotokozera za cipiringu cimene.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 19