Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 16:19-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Koma pamene ambuye ace anaona kuti kulingalira kwa kupindula kwao kwatha, anagwira Paulo ndi Sila, nawakokera kunka nao kubwalo kwa akuru,

20. ndipo pamene adanka nao kwa oweruza, anati, Anthu awa abvuta kwambiri mudzi wathu, ndiwo Ayuda,

21. ndipo alalikira miyambo imene siiloleka ife kuilandira, kapena kuicita, ndife Aroma.

22. Ndipo linagumukira iwo khamulo; ndipo oweruza anawang'ambira maraya ao; nalamulira kuti awakwapule.

23. Pamene anawaonetsa mikwingwirima yambiri, anawaika m'ndende, nauza mdindo kuti awasunge bwino.

24. Pakumva iye kulamulira kotero anawaika m'cipinda ca m'kati, namangitsa mapazi ao m'zigologolo.

25. Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Sila analinkupemphera, nayimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva;

26. ndipo mwadzidzidzi panali cibvomezi cacikuru, cotero kuti maziko a ndende anagwedezeka: pomwepo pamakomo ponse panatseguka; ndi maunyolo a onse anamasuka.

27. Pamene anautsidwa kutulo mdindoyo, anaona kuti pa makomo a ndende panatseguka, ndipo anasolola lupanga lace, nati adziphe yekha, poyesa kuti am'ndende adathawa.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 16