Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 14:4-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo khamu la mudziwo linagawikana; ena analindi Ayuda, komaena anali ndi atumwi.

5. Ndipo pamene panakhala cigumukiro ca Ahelene ndi ca Ayuda ndi akuru ao, ca kuwacitira cipongwe ndi kuwaponya miyala,

6. iwo anamva, nathawira ku midzi ya Lukaoniya, Lustra ndi Derbe, ndi dziko lozungulirapo:

7. kumeneko ndiko Uthenga Wabwino.

8. Ndipo pa Lustra panakhala munthu wina wopanda mphamvu ya m'mapazi mwace, wopunduka cibadwire, amene sanayenda nthawi zonse.

9. Ameneyo anamva Paulo alinkulankhula; ndipo Paulo pomyang'anitsa, ndi kuona kuti anali ndi cikhulupiriro colandira naco moyo,

10. anati ndi mau akuru, Taimirira. Ndipo iyeyu anazunzuka, nayenda.

11. Pamene makamu anaona cimene anacita Paulo, anakweza mau ao, nati m'cinenero ca Lukaoniya, Milungu yatsikira kwa ife monga anthu.

12. Ndipo anamucha Bamaba, Zeu; ndi Paulo, Herme, cifukwa anali wotsogola kunena.

13. Koma wansembe wa Zeu wa kumaso kwa mudzi, anadza nazo ng'ombe ndi maluwa kuzipata, nafuna kupereka nsembe pamodzi ndi makamu.

14. Pamene anamva atumwi Paulo ndi Bamaba, anang'amba zopfunda zao, natumphira m'khamu,

15. napfuula Dati, Anthuni, bwanji mucita zimenezi? ifenso tiri anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zacabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse ziri momwemo:

16. m'mibadwo, yakale iye adaleka mitundu yonse iyende m'njira mwao.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 14