Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 13:5-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo pokhala ku Salami, analalikira mau a Mulungu m'masunagoge a Ayuda; ndipo anali nayenso Yohane mnyamata wao.

6. Ndipo m'mene anapitirira cisumbu conse kufikira Pafo, anapezapo munthu watsenga, mneneri wonyenga, ndiye Myuda, dzina lace Baryesu;

7. ameneyo anali ndi kazembe Sergio Paulo, ndiye munthu wanzeru. Yemweyo anaitana Barnaba ndi Saulo, nafunitsa kumva mau a Mulungu.

8. Koma Elima watsengayo (pakuti dzina lace litera posandulika) anawakaniza, nayesa kupatutsa kazembe asakhulupire.

9. Koma Saulo, ndiye Paulo, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anampenyetsetsa iye,

10. nati, Wodzala ndi cinyengo conse ndi cenjerero lonse, iwe, mwana wa mdierekezi, mdani wa cilungamo conse, kodi sudzaleka kuipsa njira zolunjika za Ambuye?

11. Ndipo tsopano, taona, dzanja la Ambuye liri pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu wosapeoya dzuwa nthawi, Ndipo pomwepo lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo anamukamoka oaf una wina womgwira dzanja.

12. Pamenepo kazembe, pakuona cocitikacoanakhulupira, nadabwa naco ciphunzitso ca Ambuye.

13. Ndipo atamasula kucokera ku Pafo a ulendo wace wa Paulo anadza ku Perge wa ku Pamfuliya; koma Yohane anapatukana nao nabwerera kunka ku Yerusalemu.

14. Koma iwowa, atapita pocokera ku Perge anafika ku Antiokeya wa m'Pisidiya; ndipo analowa m'sunagoge tsiku la Sabata, nakhala pansi.

15. Ndipo m'mene adatha kuwerenga cilamulo ndi aneneri akulu a sunagoge anatuma wina kwa iwo, ndi kunena, Amuna inu, abale, ngati muli nao mau akudandaulira anthu, nenani.

16. Ndipo Paulo ananyamuka, nakodola ndi dzanja, nati,Amuna a Israyeli, ndi inu akuopa Mulungu, mverani.

17. Mulungu wa anthu awa Israyeli anasankha makolo athu, nakweza anthuwo pakugonerera iwo m'dziko la Aigupto, ndipo ndi dzanja lokwezeka anawaturutsa iwo m'menemo.

18. Ndipo monga nthawi ya zaka makumi anai anawalekerera m'cipululu.

19. Ndipo m'mene adaononga mitundu ya anthu isanu ndi iwiri m'Kanani, anawapatsa colowa dziko lao, monga zaka mazana anai kudza makumi asanu;

20. ndipo zitatha izi anawapatsa oweruza kufikira Samueli mneneriyo.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 13