Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 13:13-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo atamasula kucokera ku Pafo a ulendo wace wa Paulo anadza ku Perge wa ku Pamfuliya; koma Yohane anapatukana nao nabwerera kunka ku Yerusalemu.

14. Koma iwowa, atapita pocokera ku Perge anafika ku Antiokeya wa m'Pisidiya; ndipo analowa m'sunagoge tsiku la Sabata, nakhala pansi.

15. Ndipo m'mene adatha kuwerenga cilamulo ndi aneneri akulu a sunagoge anatuma wina kwa iwo, ndi kunena, Amuna inu, abale, ngati muli nao mau akudandaulira anthu, nenani.

16. Ndipo Paulo ananyamuka, nakodola ndi dzanja, nati,Amuna a Israyeli, ndi inu akuopa Mulungu, mverani.

17. Mulungu wa anthu awa Israyeli anasankha makolo athu, nakweza anthuwo pakugonerera iwo m'dziko la Aigupto, ndipo ndi dzanja lokwezeka anawaturutsa iwo m'menemo.

18. Ndipo monga nthawi ya zaka makumi anai anawalekerera m'cipululu.

19. Ndipo m'mene adaononga mitundu ya anthu isanu ndi iwiri m'Kanani, anawapatsa colowa dziko lao, monga zaka mazana anai kudza makumi asanu;

20. ndipo zitatha izi anawapatsa oweruza kufikira Samueli mneneriyo.

21. Ndipo kuyambira pamenepo anapempha mfumu; ndipo Mulungu anawapatsa Sauli mwana wa Kisi, munthu wa pfuko la Benjamini, zaka makumi anai.

22. Ndipo m'mene atamcotsa iye, anawautsira Davine akhale mfumu yao; amenenso anamcitira umboni, nati, Ndapeza Davine, mwana wa Jese, munthu wa pamtima panga, amene adzacita cifuniro canga conse.

23. Wocokera mu mbeu yace Mulungu, monga mwa lonjezano, anautsira Israyeli Mpulumutsi, Yesu;

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 13