Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 12:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma nyengo imeneyo Herode mfumu anathira manja ena a m'Eklesia kuwacitira zoipa.

2. Ndipo adapha ndi lupanga Yakobo a mbale wa Yohane.

3. Ndipo pakuona kuti kudakondweretsa Ayuda, anaonjezapo nagwiranso Petro. Ndipo awo ndi masiku a mkate wopanda cotupitsa.

4. Ndipo m'mene adamgwira, anamuika m'ndende, nampereka kwa magulu anai a alonda, lonse anai anai, amdikire iye; ndipo anafuna kumturutsa kudza naye kwa anthu atapita Paskha.

5. Pamenepo ndipo Petro anasungika m'ndende; koma Eklesia anampempherera iye kwa Mulungu kosalekeza.

6. Ndipo pamene Herode anati amturutse, usiku womwewo Petro analikugona pakati pa asilikari awiri, womangidwa ndi maunyolo awiri; ndipo alonda akukhalapakhomoanadikira ndende.

7. Ndipo taonani, mngelo wa Ambuye anaimirirapo, ndipo kuunika kunawala mokhalamo iye; ndipo anakhoma Petro m'nthiti, namuutsa iye, nanena, Tauka msanga, Ndipo maunyolo anagwa kucoka m'manja mwace.

8. Ndipo mngelo anati kwa iye, Dzimangire m'cuuno, numange nsapato zako. Nacita cotero. Ndipo ananena naye, Pfunda cobvala cako, nunelitsate ine.

9. Ndipo anaturuka, namtsata; ndipo sanadziwa kuti ncoona cocitidwa ndi mngelo, koma anayesa kuti alikuona masomphenya.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 12