Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 10:8-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. ndipo m'mene adawafotokozerazonse, anawatuma ku Yopa.

9. Koma m'mawa mwace, pokhala paulendo pao iwowa, m'mene anayandikira mudzi, Petro anakwera pachindwi kukapemphera, ngati pa ora lacisanu ndi cimodzi; ndipo anagwidwa njala, nafuna kudya;

10. koma m'mene analikumkonzera cakudya kudamgwera ngati kukomoka;

11. ndipo anaona pathambo padatseguka, ndi cotengera cirinkutsika, conga ngati cinsaru cacikuru, cogwiridwa pa ngondya zace zinai, ndi kutsikira padziko pansi;

12. m'menemo munali nyama za miyendo inai za mitundu yonse, ndi zokwawa za padziko ndi mbalame za m'mlengalenga.

13. Ndipo anamdzera mau, Tauka, Petro; ipha, nudye.

14. Koma Petro anati, Iaitu, Mbuye; pakuti sindinadya ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa.

15. Ndipo mau anamdzeranso nthawi yaciwiri, Cimene Mulungu anayeretsa, usaciyesa cinthu wamba.

16. Ndipo cinacitika katatu ici; ndipo pomwepo cotengeraco cinatengedwa kunka kumwamba.

17. Ndipo pokayika-kayika Petro mwa yekha ndi kuti masomphenya adawaona akuti ciani, taonani, amuna aja otumidwa ndi Komeliyo, atafunsira nyumba ya Simoni, anaima pa cipata,

18. ndipo anaitana nafunsa ngati Simoni, wochedwanso Petro, acerezedwako.

19. Ndipo m'mene Petro analingirira za masomphenya, Mzimu ananena naye, Taona, amuna atatu akufuna iwe.

20. Komatu tauka, nutsike, ndipo upite nao, wosakayika-kayika; pakuti ndawatuma ndine.

21. Ndipo Petro anatsikira kwa anthuwo, nati, Taonani, ine ndine amene mumfuna; cifukwa cace mwadzera nciani?

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 10