Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 10:22-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo anati, Komeliyo kenturiyoyo, munthu wolungama ndi wakuopa Mulungu, amene mtundu wonse wa Ayuda umcitira umboni, anacenjezedwa ndi mngelo woyera kuti atumize nakuitaneni mumuke ku nyumba yace, ndi kummvetsa mau anu.

23. Pamenepo anawalowetsa nawacereza.Ndipo m'mawa mwace ananyamuka naturuka nao, ndi ena a abale a ku Yopaanamperekezaiye.

24. Ndipo m'mawa mwace analowa m'Kaisareya, Koma Komeliyo analikudikira iwo, atasonkhanitsa abale ace ndi mabwenzi ace eni eni.

25. Ndipo panali pakulowa Petro, Komeliyo anakomana naye, nagwa pa mapazi ace, namlambira.

26. Koma Petro anamuutsa iye, nanena, Nyamuka; inenso ndine munthu.

27. Ndipo pakukamba naye, analowa, napeza ambiri atasonkhana;

28. ndipo anati kwa iwo, Mudziwa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina; koma Mulungu anandionetsera ine ndisanenere ali yense ali munthu wamba kapena wonyansa;

29. cifukwa cacenso ndinadza wosakana, m'mene munatuma kundiitana. Pamenepo ndifunsa, mwandiitaniranji?

30. Ndipo Komeliyo anati, Atapita masiku anai, kufikira monga ora ili, ndinalikupemphera m'nyumba yanga pa ora lacisanu ndi cinai; ndipo taonani, padaimirira pamaso panga munthu wobvala cobvala conyezimira,

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 10