Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 8:43-56 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

43. Ndipo mkazi, anali ndi nthenda yacidwalire zaka khumi ndi ziwiri, amene adasudzula asing'anga za moyo wace zonse, ndipo sanathe kuciritsidwa ndi mmodzi yense,

44. anadza pambuyo pace, nakhudza mphonje yacobvala cace; ndipo pomwepo nthenda yace inaleka.

45. Ndipo Yesu anati, Wandikhudza Ine ndani? Koma pamene onse anakana, Petro ndi iwo akukhala naye anati, Ambuye, anthu aunyinji alikukankhana pa Inu ndi kukanikizana.

46. Koma Yesu anati, Wina wandikhudza Ine; pakuti a ndazindikira Ine kuti mphamvu yaturuka mwa Ine.

47. Ndipo mkaziyo pakuona kuti sanabisika, anadza ndi kunthunthumira, nagwa pamaso pace, nafotokoza pamaso pa anthu onsewo cifukwa cace ca kumkhudza iye, ndi kuti anaciritsidwa pomwepo.

48. Ndipo iye anati kwa iyeyu, Mwana wanga, cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.

49. M'mene iye anali cilankhulire, anadza wina wocokera kwa mkuru wa sunagoge, nanena, Mwana wako wafa; usambvute Mphunzitsi.

50. Koma Yesu anamva, namyankha, kuti, Usaope; khulupira kokha, ndipo iye adzapulumutsidwa.

51. Ndipo pakufika iye kunyumbako, sanaloleza wina kulowa naye pamodzi, koma Petro, ndi Yohane, ndi Yakobo, ndi atate wa mwanayo, ndi amace.

52. Ndipo anthu onse analikumlira iye ndi kudzigugudapacifuwa. Koma iye anati, Musalire; pakuti iye sanafa, koma agona tulo.

53. Ndipo anamseka iye pwepwete podziwa kuti anafa.

54. Ndipo iye anamgwira dzanja lace, naitana, nati, Buthu, tauka.

55. Ndipo mzimu wace unabwera, ndipo anauka pomwepo; ndipo iye anawauza kuti ampatse kanthu ka kudya.

56. Ndipo atate wace ndi amace anadabwa; ndipo analamulira iwo asauze munthu ali yense cimene cinacitika.

Werengani mutu wathunthu Luka 8