Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 7:22-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Mukani, muuze Yohane zimene mwaziona, nimwazimva; anthu akhungu alandira kuona kwao, opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.

23. Ndipo wodala iye amene sakhomudwa cifukwa ca Ine.

24. Ndipo atacoka amithenga ace a Yohane, iye anayamba kunena za Yohane kwa anthu a makamu aja, nati, Munaturuka kunka kucipululu kukapenya ciani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?

25. Koma munaturuka kukaona ciani? Munthu wobvala zobvala zofewa kodi? Onani, iwo akubvala zolemera, ndi akukhala odyerera, ali m'makuka a mafumu.

26. Koma munaturuka kukaona ciani? Mneneri kodi? Etu, ndinena kwa inu, ndipo wakuposa mneneri.

27. Uyu ndi iye amene kunalembedwa za iye,Ona, ndituma Ine mthenga wanga akutsogolere,Amene adzakukonzera njira yako pamaso pako.

28. Ndinena kwa inu, kuti, Mwa akubadwa ndi akazi palibe mmodzi wamkuru woposa Yohane; koma iye amene ali wamng'ono mu Ufumu wa Mulungu amposa iye.

29. Ndipo anthu onse ndi amisonkho omwe, pakumva, anabvomereza kuti Mulungu ali wolungama, popeza anabatizidwa iwo ndi ubatizo wa Yohane.

30. Koma Afarisi ndi acilamulo anakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo okha, popeza sanabatizidwa ndi iye.

31. Ndipo, ndidzafanizira ndi ciani anthu a mbadwo uno? ndipo afanana ndi ciani?

32. Angofanana ndi ana akukhala pamsika, ndi kuitanizana wina ndi mnzace, ndi kunena, Ife tinakulizirani citoliro, ndipo inu simunabvina ai; tinabuma maliro, ndimo simunalira ai.

33. Pakuti Yohane Mbatizi wafika wosadya mkate ndi wosamwa vinyo; ndipo munena, Ali ndi ciwanda.

34. Mwana wa munthu wafika wakudya ndi wakumwa; ndipo munena, Onani, munthu wosusuka ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi anthu ocimwa!

35. Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ana ace onse.

36. Ndipo mmodzi wa Afarisi anamuitana iye kuti akadye naye. Ndipo analowa m'nyumba ya Mfarisi, naseama pacakudya.

37. Ndipo onani, mkazi wocimwa, amene anali m'mudzimo; ndipo pakudziwa kuti Yesu analikuseama pacakudya m'nyumba ya Mfarisi, anatenga nsupa yaalabastero ya mafuta onunkhira bwino,

38. naimirira kumbuyo, pa mapazi ace, nalira, nayamba kukhathamiza mapazi ace ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi la mutu wace, nampsompsonetsa mapazi ace, nawadzoza ndi mafuta onunkhira bwino.

39. Koma Mfarisi, amene adamuitana iye, pakuona, ananena mwa yekha, nati, Akadakhala mneneri uyu akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo womkhudza iye, cifukwa ali wocimwa.

40. Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Simoni, ndiri ndi kanthu kakunena kwa iwe. Ndipo iye anabvomera, Mphunzitsi, nenani.

41. Munthu wokongoletsa ndalama anali nao amangawa awiri; mmodziyo anali ndi mangawa ace a marupiya mazana asanu, koma mnzace makumi asanu.

42. Popeza analibe cobwezera iwo, anawakhululukira onse awiri. Cotero, ndani wa iwo adzaposa kumkonda?

Werengani mutu wathunthu Luka 7