Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 6:43-49 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

43. Pakuti 11 palibe mtengo wabwino wakupatsa zipatso zobvunda; kapenanso mtengo woipa wakupatsa zipatso zabwino,

44. Pakuti 12 mtengo uli wonse uzindikirika ndi cipatso cace. Pakuti anthu samachera nkhuyu paminga, kapena pamtungwi samachera mphesa,

45. 13 Munthu wabwino aturutsa zabwino m'cuma cokoma ca mtima wace; ndi munthu woipa aturutsa zoipa m'coipa cace: pakuti m'kamwa mwace mungolankhula mwa kucuruka kwa mtima wace.

46. Ndipo 14 mundichuliranji Ine, Ambuye, Ambuye, ndi kusacita zimene ndizinena?

47. 15 Munthu ali yense wakudza kwa Ine, ndi kumva mau anga, ndi kuwacita, ndidzakusonyezani amene afanana naye.

48. Iye afanafana ndi munthu wakumanga nyumba, amene anakumba pansi ndithu, namanga maziko a nyumbayo pathanthwe; ndipo pamene panadza cigumula, mtsinje unagunda pa nyumbayo, ndipo sunakhoza kuigwedeza; cifukwa idamangika bwino.

49. Koma iye amene akumva, ndi kusacita, afanafana ndi munthu wakumanga nyumba pa nthaka yopanda maziko; pa imeneyo unagunda mtsinje, ndipo inagwa pomwepo; ndipo kugumuka kwace kwa nyumbayo kunali kwakukuru.

Werengani mutu wathunthu Luka 6