Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 5:4-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo pamene iye analeka kulankhula, anati kwa Simoni, Kankhira kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza.

5. Ndipo Simoni anayankha, nati, Ambuye, tinagwiritsa nchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mau anu ndidzaponya makoka.

6. Ndipo pamene anacita ici, anazinga unyinji waukuru wansomba; ndipo makoka ao analinkung'ambika;

7. ndipo anakodola anzao a m'ngalawa yinayo, adze awathangate. Ndipo anadza, nadzaza ngalawa zonse ziwiri, motero kuti zinalinkumira.

8. Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mabondo ace a Yesu, nanena, Mucoke kwa ine, Ambuye, cifukwa ndine munthu wocimwa.

9. Pakuti cizizwo cidagwira iye, ndi onse amene anali naye, pa kusodzako kwa nsomba zimene anazikola;

10. ndipo cimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, amene anali anzace a Simoni. Ndipo Yesu anati kwa Simoni, Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.

11. Ndipo m'mene iwo anakoceza ngalawa zao pamtunda, anasiya zonse, namtsata iye.

12. Ndipo panali, pamene iye anali m'mudzi wina, taona, munthu wodzala ndikhate; ndipopameneanaona Yesu, anagwa nkhope yace pansi, nampempha iye, nanena, Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza.

13. Ndipo iye anatambalitsa dzanja lace, namkhudza, nanena, Ndifuna, takonzeka, Ndipo pomwepo khate linacoka kwa iye.

Werengani mutu wathunthu Luka 5