Ndipo iye analowa m'ngalawa imodzi, ndiyo yace ya Simoni, nampempha iye akankhe pang'ono. Ndipo anakhala pansi m'menemo, naphunzitsa m'ngalawa makamuwo a anthu.