Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 4:38-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

38. Ndipo iye ananyamuka kucokera m'sunagoge, nalowa m'nyumba ya Simoni. Koma momwemo munali mpongozi wace wa Simoni, anagwidwa ndi nthenda yolimba yamalungo; ndipo anampempha Yesu za iye.

39. Ndipo iye anaimirira, naweramira pa iye, nadzudzula nthendayo; ndipo inamleka iye: ndipo anauka msangatu, nawatumikira.

40. Ndipo pakulowa dzuwa anthu onse amene anali nao odwala ndi nthenda za mitundu mitundu, anadza nao kwa iye; ndipo iye anaika manja ace pa munthu ali yense wa iwo, nawaciritsa.

41. Ndi ziwanda zomwe zinaturuka mwa ambiri, ndi kupfuula, kuti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. Ndipo iye anazidzudzula, wosazilola kulankhula, cifukwa zinamdziwa kuti iye ndiye Kristu.

42. Ndipo kutaca anaturuka iye nanka ku malo acipululu; ndi makamu a anthu analikwnfunafuna iye, nadza nafika kwa iye, nayesa kumletsa iye, kuti asawacokere.

43. Koma anati kwa iwo, Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ku midzi yinanso: cifukwa ndinatumidwa kudzatero.

44. Ndipo iye analikulalikira m'masunagoge a ku Galileya.

Werengani mutu wathunthu Luka 4