Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 4:14-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo Yesu anabwera ndi mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mbiri yace ya iye inabuka ku dziko lonse loyandikira.

15. Ndipo iye anaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalemekezedwa ndi anthu onse.

16. Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analowa m'sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m'kalata.

17. Ndipo anapereka kwa iye buku la Yesaya mneneri. Ndipo m'mene iye adafunyulula bukulo, anapeza pomwe panalembedwa,

18. Mzimu wa Ambuye uli paine,Cifukwa cace iye anandidzozaIne ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino:Anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe,Ndi akhungu kuti apenyenso,Kuturutsa ndi ufuru ophwanyika,

19. Kulalikira caka cosankhika ca Ambuye.

20. Ndipo m'mene iye anapinda bukulo, nalipereka kwa mnyamata, anakhala pansi; ndipo maso ao a anthu onse m'sunagogemo anamyang'anitsa iye.

21. Ndipo anayamba kunena kwa iwo, kuti, Lero lembo ili lakwanitsidwa m'makutu anu.

22. Ndipo onse anamcitira iye umboni nazizwa ndi mau a cisomo akuturuka m'kamwa mwace; nanena, Kodi uyu si mwana wa Yosefe?

23. Ndipo anati kwa iwo, Kwenikweni mudzati kwa Ine nkhani iyi, Sing'anga iwe, tadziciritsa wekha: zonse zija tazimva zinacitidwa ku Kapernao, muzicitenso zomwezo kwanu kuno.

24. Ndipo iye anati, Indetu, ndinena kwa inu, kuti, Palibe mneneri alandirika ku dziko la kwao.

25. Koma zoonadi ndinena kwa inu, kuti, Munali akazi amasiye ambiri m'lsrayeli masiku ace a Eliya, pamene kunatsekedwa kumwamba zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, pamene panakhala njala yaikuru pa dziko lonselo;

Werengani mutu wathunthu Luka 4