Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 3:9-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo; cotero mtengo uli wonse wosabala cipatso cabwino udulidwa, nuponyedwa pamoto.

10. Ndipo anthu a makamu anamfunsa iye, nanena, Ndipo tsono tizicita ciani?

11. Koma iye anayankha nanena kwa iwo, Iye amene ali nao malaya awiri apatse kwa iye amene alibe; ndi iye amene ali nazo zakudya acite comweco.

12. Ndipo amisonkho omwe anadza kudzabatizidwa, nati kwa iye, Mphunzitsi, ife tizicita ciani?

13. Koma iye anati kwa iwo, Musakapambe kanthu konse kakuposa cimene anakulamulirani.

14. Ndipo asilikari omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizicita ciani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu ali yense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu.

15. Ndipo pamene anthu anali kuyembekezera, ndipo onse anaganizaganiza m'mitima yao za Yohane, ngati kapena iye ali Kristu;

16. Yohane anayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula lamba la nsapato zace; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:

Werengani mutu wathunthu Luka 3