Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 23:26-45 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo popita naye, anagwira munthu, Simoni wa ku Kurene, alikucokera kuminda, namsenza iye mtanda aunyamule pambuyo pace pa Yesu,

27. Ndipo unamtsata unyinji waukuru wa anthu, ndi wa akazi amene anadziguguda pacifuwa, namlirira iye.

28. Koma Yesu anawapotolokera nati, Ana akazi inu a Yerusalemu, musandilirire Ine, koma mudzilirire nokha ndi ana anu.

29. Cifukwa taonani masiku alinkudza, pamene adzati, Odala ali ouma ndi mimba yosabala, ndi mawere osayamwitsa.

30. Pomwepo adzayamba kunena kwa mapiri, Igwani pa ife; ndi kwa zitunda, Bisani ife.

31. Pakuti ngati azicitira izi mtengo wauwisi, nanga kudzatani ndi wouma?

32. Ndipo analinso awiri ena, ndiwo ocita zoipa; anatengedwa pamodzi ndi iye kuti aphedwe.

33. Ndipo pamene anafika ku malo dzina lace Bade, anampacika iye pamtanda pomwepo, ndi ocita zoipa omwe, mmodzi ku dzanja lamanja ndi wina kulamanzere.

34. Ndipo Yesu ananena, Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa cimene acita. Ndipo anagawana zobvala zace, poyesa maere.

35. Ndipo anthu anaima alikupenya, Ndi akurunso anamlalatira iye nanena, Anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati iye ndiye Kristu wa Mulungu, wosankhidwa wace.

36. Ndipo asilikarinso anamnyoza, nadza kwa iye, nampatsa vinyo wosasa,

37. nanena, Ngati Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda, udzipulumutse wekha.

38. Ndipo kunalinso lembo pamwamba pace, ndilo: UYU NDIYE MFUMU YAAYUDA.

39. Ndipo mmodzi wa ocita zoipa anapacikidwawo anamcitira iye mwano nanena, Kodi suli Kristu Iwe? udzipulumutse wekha ndi ife.

40. Koma winayo anayankha, namdzudzula iye, nati, Kodi suopa Mulungu, poona uli m'kulangika komweku?

41. Ndipo ifetu kuyenera; pakuti tirikulandira zoyenera zimene tinazicita: koma munthu uyu sanacita kanthu kolakwa.

42. Ndipo ananena, Yesu, ndikumbukileni m'mene mulowa Ufumuwanu.

43. Ndipo Iye ananena naye, Indetu, ndinena ndi iwe, Lero lino udzakhala ndine m'Paradaiso.

44. Ndipo ora lace pamenepo linali ngati lacisanu ndi cimodzi. Ndipo panali mdima pa dziko lonse kufikira ora lacisanu ndi cinai, ndipo dzuwa linada.

45. Ndipo nsaru yocinga ya m'Kacisi inang'ambika pakati.

Werengani mutu wathunthu Luka 23