Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 21:5-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo pamene ena analikunena za Kacisiyo, kuti anakonzeka ndi miyala yokoma ndi zopereka, anati iye,

6. Zinthu izi muziona, adzafika masiku, pamenepo sudzasiyidwa pano mwala pa mwala unzace, umene sudzagwetsedwa.

7. Ndipo iwo anamfunsa iye, nati, Mphunzitsi, nanga zinthu izi zidzaoneka liti? ndipo cizindikilo ndi cianipamene izi ziti zicitike?

8. Ndipo iye anati, Yang'anirani musasoceretsedwe; pakuti ambiri adzadza m'dzina langa, nadzanena, Ndine amene; ndipo, Nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pao.

9. Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi mapanduko, musaopsedwa; pakuti ziyenera izi ziyambe kucitika; koma mathedwe sakhala pomwepo.

10. Pamenepo ananena nao, Mtundu wa anthu udzaukira pa mtundu wina, ndipo ufumu pa ufumu wina:

11. ndipo kudzakhala zibvomezi zazikuru, ndi njala ndi miliri m'malo akutiakuti, ndipo kudzakhala zoopsya ndi zizindikilo zazikuru zakumwamba.

12. Koma zisanacitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, cifukwa ca dzina langa.

13. Kudzakhala kwa inu ngati umboni.

14. Cifukwa cace tsimikizani mumtima mwanu, kuti usanafike mlandu musalingirire cimene mudzayankha.

15. Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.

16. Koma mudzaperekedwa ngakhale ndi akukubalani, ndi abale, ndi a pfuko lanu, ndi abwenzi anu; ndipo ena a inu adzakuphani,

17. Ndipo anthu onse adzadana ndi inu cifukwa ca dzina langa.

18. Ndipo silidzaonongeka tsitsi limodzi la pamutu panu.

19. Mudzakhala nao moyo wanu m'cipiriro.

20. Koma pamene pali ponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti cipululutso cace cayandikira.

21. Pamenepo iwo ali m'Yudeya athawire kumapiri, ndi iwo ali m'kati mwa uwo aturuke, ndi iwo ali kumiraga asalowemo.

22. Cifukwa amenewa ndi masiku akubwezera, kuti zonse zidalembedwa zicitike.

23. Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi iwo akuyamwitsa ana masiku awo! pakuti padzakhala cisauko cacikuru padziko, ndi mkwiyo pa anthu awa.

Werengani mutu wathunthu Luka 21