Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 18:19-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Koma Yesu anati kwa iye, Undicha Ine wabwino bwanji? palibe wabwino, koma mmodzi, ndiye Mulungu.

20. Udziwa malamulo. Usacite cigololo, Usaphe, Usabe, Usacite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amako.

21. Koma anati, Izi zonse ndazisunga kuyambira ubwana wanga.

22. Koma m'mene Yesu anamva, anati kwa iye, Usowa cinthu cimodzi: gulitsa ziri zonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala naco cuma ceni ceni m'Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.

23. Koma pakumva izi anagwidwa naco cisoni cambiri; pakuti anali mwini cuma cambiri.

24. Ndipo Yesu pomuona iye anati, Ha! nkubvutika nanga kwa anthu eni cuma kulowa Ufumu wa Mulungu!

25. Pakuti nkwapafupi kwa ngamila apyole diso la singano koma kwa munthu mwini cuma, kulowa Ufumu wa Mulungu nkwapatali.

26. Koma akumvawo anati, Tsono ndani angathe kupulumutsidwa?

27. Koma iye anati, Zinthu zosatheka ndi anthu zitheka ndi Mulungu.

28. Ndipo Petro anati, Taonani ife tasiya zathu za ife eni, ndipo takutsatani Inu.

29. Koma anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Palibe munthu wasiya nyumba, kapena mkazi, kapena abale, kapena akumbala, kapena ana, cifukwa ca Ufumu wa Mulungu,

30. koma adzalandira zobwezedwa koposatu m'nthawi yino; ndipo m'nthawi irinkudza moyo wosatha.

Werengani mutu wathunthu Luka 18