Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 16:7-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Pomwepo anati kwa wina, Ndipo iwe uli nao mangawa otani? Ndipo uyu anati, Mitanga ya tirigu zana iye ananena naye, Tenga kalata wako nulembere makumi asanu ndi atatu.

8. Ndipo mbuye wace anatama kapitao wonyengayo, kuti anacita mwanzeru; cifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m'mbadwo wao koposa ana a kuunika.

9. Ndipo Ine ndinena kwa inu, Mudziyesere nokha abwenzi ndi cuma cosalungama; kuti pamene cikakusowani, iwo akalandire inu m'mahema osatha.

10. Iye amene akhulupirika m'cacing'onong'ono alinso wokhulupirika m'cacikuru; ndipo iye amene ali wosalungama m'cacing'onong'ono alinso wosalungama m'cacikuru.

11. Cifukwa cace ngati simunakhala okhulupirika m'cuma ca cosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi cuma coona?

12. Ndipo ngati simunakhala okhulupirika ndi zace za wina, adzakupatsani inu ndani za inu eni?

13. Palibe mnyamata wa m'nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Cuma.

14. Koma Marisi, ndiwo okonda ndalama, anamva izi zonse; ndipo anamseka.

15. Ndipo anati kwa iwo, Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; cifukwa ici cimene cikuzika mwa anthu ciri conyansa pamaso pa Mulungu.

16. Cilamulo ndi aneneci analipo kufikira pa Yohane; kuyambira pamenepo ulalikidwa Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndipo munthu ali yense akangamira kulowamo.

17. Kuti kumwamba ndi dziko lapansi zicoke nkwapafupi, koma kuti kalembo kakang'ono ka cilamulo kagwe nkwapatali.

18. Yense wakusudzula mkazi wace, nakwatira wina, acita cigololo; ndipo iye amene akwatira wosudzulidwayo, acita cigololo,

19. Ndipo panali munthu mwini cuma amabvala cibakuwa ndi nsaru yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse;

20. ndipo wopemphapempha wina, dzina lace Lazaro, adaikidwa pakhomo pace wodzala ndi zironda,

21. ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini cumayo; komatu agarunso anadza nanyambita zirondazace.

Werengani mutu wathunthu Luka 16