Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 15:4-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Munthu ndani wa inu ali nazo nkhosa makumikhumi, ndipo pakutayika imodzi ya izo, sasiya nanga m'cipululu zinazo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai, nalondola yotayikayo kufikira aipeza?

5. Ndipo pamene adaipeza, aisenza pa mapewa ace wokondwera.

6. Ndipo pakufika kunyumba kwace amema abwenzi ace ndi anansi ace, nanena nao, Kondwerani ndi ine, cifukwa ndinapeza nkhosa yanga yotayikayo.

7. Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala cimwemwe Kumwamba cifukwa ca wocimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.

8. Kapena mkazi wanji ali nazo ndalama zasiliva khumi, ngati itayika imodzi, sayatsa nyali, nasesa m'nyumba yace, nafunafuna cisamalire kufikira akaipeza?

9. Ndipo m'mene aipeza amema abwenzi ace ndi anansi ace, nanena; Kondwerani ndi ine, cifukwa ndinapeza ndalama ndidatayayo.

10. Comweco, ndinena kwa inu, kuli cimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu cifukwa ca munthu wocimwa mmodzi amene atembenuka mtima.

11. Ndipo iye anati, Munthu wina anali ndi ana amuna awiri;

12. ndipo wamng'onoyo anati kwa atate wace, Atate, ndigawirenitu zanga za pa cuma canu. Ndipo iye anawagawira za moyo wace.

13. Ndipo pakupita masiku owerengekamwana wamng'onoyo anasonkhanitsa zonse, napita ulendo wace ku dziko lakutari; ndipo komweko anamwaza cuma cace ndi makhalidwe a citayiko.

14. Ndipo pamene anatha zace zonse, panakhala njala yaikuru m'dziko muja, ndipo iye anayamba kusowa.

15. Ndipo anamuka nadziphatikiza kwa mfulu imodzi ya dziko lija; ndipo uyu anamtumiza kubusa kwace kukaweta nkhumba.

16. Ndipo analakalaka kukhutitsa mimba yace ndi makoko amene nkhumba rimadya, ndipo palibe munthu anamninkha kanthu.

17. Koma m'mene anakumbukila mumtima, anati, Anchito olipidwa ambiri a atate wanga ali naco cakudya cocuruka, ndipo ine ndionongeke kuno ndi njala?

18. Ndidzanyamuka ndipite kwa atate wanga, ndipo ndidzanena nave, Atate, ndinacimwira Kumwamba ndi pamaso panu;

19. sindiyeneranso konse kuchulidwa mwana wanu; mundiyese ine ngati mmodzi wa anchito anu.

20. Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wace. Koma pakudza iye kutali, atate wace anamuona, nagwidwa cifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pace, nampsompsonetsa.

21. Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinacimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kuchulidwa mwana wanu.

Werengani mutu wathunthu Luka 15