Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 14:9-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. ndipo pakufika iye amene adaitana iwe ndi uyu, adzati kwa iwe, Mpatse uyu malo; ndipo pomwepo udzayamba manyazi kukhala pa mpando wa kuthungo.

10. Koma pamene pali ponse waitanidwa iwe, pita nukhale pansi pa malo a kuthungo; kotero kuti pamene akadza iye anakuitana iwe, akanena ndi iwe, Bwenzi langa, sendera, kwera kuno; pomwepo udzakhala ndi ulemerero pamaso pa onse akuseama pacakudya pamodzi ndi iwe.

11. Cifukwa munthu ali yense wakudzikuza adzacepetsedwa; ndipo wakudzicepetsa adzakulitsidwa.

12. Ndipo ananenanso kwa iye amene adamuitana, Pamene ukonza cakudya ca pausana kapena ca madzulo, usaitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a pfuko lako, kapena anansi ako eni cuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuitana iwe, ndipo udzakhala nayo mphotho.

13. Koma pamene ukonza phwando uitane aumphawi, opunduka, otsimphina, akhungu;

14. ndipo udzakhala wodala; cifukwa iwo alibe cakubwezera iwe mphotho; pakuti idzabwezedwa mphotho pa kuuka kwa oiungama.

Werengani mutu wathunthu Luka 14