Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 14:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali pamene iye analowa m'nyumba ya mmodzi wa akuru a Afarisi tsiku la Sabat a, kukadya, iwo analikumzonda iye.

2. Ndipo onani, panali pamaso pace munthu wambulu.

3. Ndipo Yesu anayankha nati kwa acilamulo ndi Afarisi, nanena, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuciritsa, kapena iai?

4. Koma iwo anakhala cete. Ndipo anamtenga namciritsa, namuuza apite.

5. Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu buru wace kapena ng'ombe yace itagwa m'citsime, ndipo sadzaiturutsa pomwepo tsiku la Sabata kodi?

6. Ndipo iwo sanathe kumbwezera mau pa zinthu izi.

7. Ndipo iye ananena fanizo kwa oitanidwa, popenya kuti amadzisankhira mipando yaulemu, nanena kwa iwo,

8. Pamene pali ponse waitanidwa iwe ndi munthu ku cakudya ca ukwati, usaseama pa mpando waulemu; kuti kapena wina waulemu wakuposa iwe akaitanidwe ndi iye,

9. ndipo pakufika iye amene adaitana iwe ndi uyu, adzati kwa iwe, Mpatse uyu malo; ndipo pomwepo udzayamba manyazi kukhala pa mpando wa kuthungo.

10. Koma pamene pali ponse waitanidwa iwe, pita nukhale pansi pa malo a kuthungo; kotero kuti pamene akadza iye anakuitana iwe, akanena ndi iwe, Bwenzi langa, sendera, kwera kuno; pomwepo udzakhala ndi ulemerero pamaso pa onse akuseama pacakudya pamodzi ndi iwe.

11. Cifukwa munthu ali yense wakudzikuza adzacepetsedwa; ndipo wakudzicepetsa adzakulitsidwa.

12. Ndipo ananenanso kwa iye amene adamuitana, Pamene ukonza cakudya ca pausana kapena ca madzulo, usaitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a pfuko lako, kapena anansi ako eni cuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuitana iwe, ndipo udzakhala nayo mphotho.

Werengani mutu wathunthu Luka 14