Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 13:7-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo anati kwa wosungira munda wamphesa, Taona, zaka zapita zitatu ndimadza ine kudzafuna cipatso pa mkuyu uwu, ndipo ndimapeza palibe: taulikha; uyeseranjinso nthaka yopanda pace?

8. Ndipo iye anayankha nanena naye, Mbuye, baulekani ngakhale caka cino comwe, kufikira ndidzaukumbira kwete, ndithirepo ndowe;

9. ndipo, ngati udzabala cipatso kuyambira pamenepo, cabwino; koma ngati iai, mudzaulikhatu.

10. Ndipo analikuphunzitsa m'sungagoge mwina, tsiku la Sabata.

11. Ndipo mkazi anali nao mzimu wakumdwalitsa zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu; nakhala wopeteka, ndimo analibe mphamvu konse yakuweramuka.

12. Ndipo Yesu m'mene anamuona, anamuitana, nanena naye, Mkaziwe, wamasulidwa kudwala kwako.

13. Ndipo anaika manja ace pa iye; ndipo pomwepo anaongoledwa, nalemekeza Mulungu.

14. Ndipo mkuru wa sunagoge anabvutika mtima, cifukwa Yesu anaciritsa tsiku la Sabata, nayankha, nanena kwa khamulo, Alipo masiku asanu ndi limodzi, m'menemo anthu ayenera kugwira nchito, cifukwa cace idzani kudzaciritsldwa momwemo, koma tsiku la Sabata ai.

15. Koma Ambuye anamyankha iye, nati, Onyenga inu, kodi munthu ali yense wa inu samaimasula ng'ombe yace, kapena buru wace kucodyeramo, tsiku la Sabata, kupita nayo kukaimwetsa madzi?

16. Ndipo mkazi uyu, ndiye mwana wa Abrahamu, amene Satana anammanga, onani, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu, nanga si kuyenera kodi, kuti amasulidwe nsinga yace imeneyi tsiku la Sabata?

Werengani mutu wathunthu Luka 13