Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 13:17-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo pamene Iye anatero, onse aja akutsutsana naye ananyazitsidwa; ndipo anthu onse a m'khamu anakondwera ndi zinthu zonse za ulemererozo zinacitidwa ndi iye.

18. Pamenepo ananena, Ufumu wa Mulungu ufanana ndi ciani? ndipo ndidzaufanizira ndi ciani?

19. Ufanana ndi kambeu kampiru, kamene munthu anatenga, nakaponya m'munda wace wace, ndipo kanamera, kanakula mtengo; ndi mbalame za m'mlengalenga zinabindikira mu nthambi zace.

20. Ndiponso anati, Ndidzafanizira Ufumu wa Mulungu ndi ciani?

21. Ufanana ndi cotupitsa mikate, cimene mkazianatenga, nacibisa mu miyeso itatu ya ufa, kufikira unatupa wonsewo,

22. Ndipo Iye anapita pakati pa mizinda ndi midzi, naphunzitsa, nayenda ulendo kunkabe ku Yerusalemu.

23. Ndipo munthu anati kwa iye, Ambuye, akupulumutsidwandiwo owerengeka kodi? Koma iye anati kwa iwo,

24. Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza; cifukwa anthu ambiri, ndikuuzani, adzafunafuna kulowamo, koma sadzakhoza.

25. Pamene atauka mwini nyumba natseka pakhomo, ndipo inu mudzayamba kuima pabwalo, ndi kugogoda pacitseko, ndi kunena, Ambuye titsegulireni ife; ndipo iye adzayankha nadzati ndi inu, Sindidziwa inu kumene mucokerako;

26. pomwepo mudzayambakunena, Ifetinadya ndi kumwa pamaso panu, ndipo munaphunzitsa m'makwalala a kwathu;

27. ndipo iye adzati, Ndinena kwa inu, sindidziwa kumene mucokera inu; cokani pa Ine, nonse akucita cosalungama,

28. Kudzakhala komweko kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzaona Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, ndi aneneri onse, mu. Ufumu wa Mulungu, koma inu nokha muturutsidwa kunja.

29. Ndipo anthu adzacokera kum'mawa, ndi kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwela, nadzakhalapansi mu Ufumu wa Mulungu.

30. Ndipo onani, alipo akuthungo amene adzakhala oyamba, ndipo alipo oyamba adzakhala akuthungo.

31. Nthawi yomweyo anadzapo Afarisi ena, nanena kwa iye, Turukani, cokani kuno; cifukwa Herode afuna kupha lou.

Werengani mutu wathunthu Luka 13