Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 13:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anakhalako nthawi yomweyo, anthu ena amene anamuuza iye za Agalileya, amene Pilato anasanganiza mwazi wao ndi nsembe zao.

2. Ndipo iye anayankha nati kwa iwo, Kodi muyesa kuti Agalileya aja anali anthu akucimwa koposa Agalileya onse, cifukwa anamva zowawa izi?

3. Ndinena kwa inu, iaitu; koma ngati inu simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse momwemo.

4. Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya m'Siloamu inawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m'Yerusalemu?

5. Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse ci, modzimodzi.

6. Ndipo iye ananena fanizo ili: Munthu wina anali ndi mkuyu wookam'munda wace wamphesa. Ndipo anadza nafuna cipatso pa uwu, koma anapeza palibe.

7. Ndipo anati kwa wosungira munda wamphesa, Taona, zaka zapita zitatu ndimadza ine kudzafuna cipatso pa mkuyu uwu, ndipo ndimapeza palibe: taulikha; uyeseranjinso nthaka yopanda pace?

8. Ndipo iye anayankha nanena naye, Mbuye, baulekani ngakhale caka cino comwe, kufikira ndidzaukumbira kwete, ndithirepo ndowe;

9. ndipo, ngati udzabala cipatso kuyambira pamenepo, cabwino; koma ngati iai, mudzaulikhatu.

10. Ndipo analikuphunzitsa m'sungagoge mwina, tsiku la Sabata.

11. Ndipo mkazi anali nao mzimu wakumdwalitsa zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu; nakhala wopeteka, ndimo analibe mphamvu konse yakuweramuka.

12. Ndipo Yesu m'mene anamuona, anamuitana, nanena naye, Mkaziwe, wamasulidwa kudwala kwako.

13. Ndipo anaika manja ace pa iye; ndipo pomwepo anaongoledwa, nalemekeza Mulungu.

Werengani mutu wathunthu Luka 13