Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 12:49-57 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

49. Ine ndinadzera kuponya mota pa dziko lapansi; ndipo ndifunanji, ngati unatha kuyatsidwa?

50. Koma ndiri ndi ubatizo ndikabatizidwe nao; ndipo ndikanikizidwa Ine kufikira ukatsirizidwa!

51. Kodi muyesa kuti ndinadzera kudzapatsa mtendere pa dziko lapani? Ndinena wa inu, Iaitu, komatu kutsutsana;

52. pakuti 6 kuyambira tsopano adzakhala m'nyumba imodzi anthu asanu, atatu adzatsutsana ndi awiri, ndi awiri adzatsutsana ndi atatu.

53. Adzatsutsana atate ndi mwana wace, ndi mwana ndi atate wace; amace adzatsutsana ndi mwana wamkazi'l ndi mwana wamkazi ndi amace, mpongozi adzatsutsana ndi mkazi wa mwana wace, ndi mkaziyo ndi mpongozi wace.

54. Koma iye ananenanso kwa makamu a anthu, 7 Pamene pali ponse muona mtambo wokwera kumadzulo, pomwepo munena, kuti, Ikudza mvula; ndipo itero.

55. Ndipo pamene mphepo ya kumwela iomba, munena, kuti, Kudzakhala kutenthatu; ndipo kuterodi.

56. Onyenga inu, mudziwa kuzindikira nkhope yace ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziwa bwanji kuzindikira nyengoyino?

57. Ndipo inunso, pa nokha mulekeranji kuweruza kolungama?

Werengani mutu wathunthu Luka 12