Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 12:26-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Kotero ngati simungathe ngakhale cacing'onong'ono, muderanji nkhawa cifukwa ca zina zija?

27. Lingalirani maluwa, makulidwe ao; sagwiritsa nchito ndi kusapota; koma ndinena kwa inu, Ngakhale Solomo, mu ulemerero wace wonse, sanabvala ngati limodzi la awa.

28. Koma ngati Mulungu abveka kotere maudzu a kuthengo akukhala lero, ndipo mawa aponyedwa pamoto; nanga inu sadzakuninkhani koposa, inu okhulupirira pang'ono?

29. Ndipo inu musafunefune cimene mudzadya, ndi cimene mudzamwa; ndipo musakayike mtima.

30. Pakuti izi zonse mitundu ya anthu a pa dziko lapansi amazifunafuna; koma Atate wanu adziwa kuti musowa zimenezi.

31. Komatu tafuna-funani Ufumu wace, ndipo izi adzakuonjezerani.

32. Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; cifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.

33. Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zacifundo; mudzikonzere matumba a ndarama amene sakutha, cuma cosatha m'Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga.

34. Pakuti kumene kuli cuma canu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.

35. Khalani odzimangira m'cuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka;

36. ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wao, pamene ati abwera kucokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo.

37. Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'cuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.

38. Ndipo akadza ulonda waciwiri, kapena wacitatu, nakawapeza atero, odala amenewa.

39. Koma zindikirani ici, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yace yakudza mbala, akadadikira, ndipo sakadalola nyumba yace ibooledwe.

40. Khalani okonzeka inunso; cifukwa nthawi imene simulingirira, Mwana wa munthu akudza.

Werengani mutu wathunthu Luka 12