Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 12:24-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Lingirirani makungubwi, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa: nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!

25. Ndipo ndani wa inu, ndi kuda nkhawa angathe kuonjeza mkono pa msinkhu wace?

26. Kotero ngati simungathe ngakhale cacing'onong'ono, muderanji nkhawa cifukwa ca zina zija?

27. Lingalirani maluwa, makulidwe ao; sagwiritsa nchito ndi kusapota; koma ndinena kwa inu, Ngakhale Solomo, mu ulemerero wace wonse, sanabvala ngati limodzi la awa.

28. Koma ngati Mulungu abveka kotere maudzu a kuthengo akukhala lero, ndipo mawa aponyedwa pamoto; nanga inu sadzakuninkhani koposa, inu okhulupirira pang'ono?

29. Ndipo inu musafunefune cimene mudzadya, ndi cimene mudzamwa; ndipo musakayike mtima.

30. Pakuti izi zonse mitundu ya anthu a pa dziko lapansi amazifunafuna; koma Atate wanu adziwa kuti musowa zimenezi.

31. Komatu tafuna-funani Ufumu wace, ndipo izi adzakuonjezerani.

32. Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; cifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.

33. Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zacifundo; mudzikonzere matumba a ndarama amene sakutha, cuma cosatha m'Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga.

34. Pakuti kumene kuli cuma canu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.

35. Khalani odzimangira m'cuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka;

36. ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wao, pamene ati abwera kucokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo.

37. Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'cuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.

Werengani mutu wathunthu Luka 12