Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 11:10-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pakuti yense wakupempha alandira; ndi wofunayo apeza; ndi iye amene agogoda adzamtsegulira.

11. Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wace akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? kapena nsomba, nadzamninkha njoka m'malo mwa nsomba?

12. kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa cinkhanira?

13. Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha iye?

14. Ndipo analikuturutsa ciwanda cosalankhula. Ndipo kunali, citaturuka ciwanda, wosalankhulayo analankhula; ndipo makamu a anthu anazizwa.

15. Koma ena mwa iwo anati, Ndi Beelzebule mkuru wa ziwanda amaturutsa ziwanda.

16. Koma ena anamuyesa, nafuna kwa iye cizindikilo cocokera Kumwamba.

17. Koma iye, podziwa zolingirira zao, anati kwa iwo, Ufumu uli wonse wogawanika m'kati mwace upasuka; ndipo nyumba ikagawanika m'kati mwace igwa.

18. Ndiponso ngati Satana agawanika kudzitsutsa mwini, udzaimika bwanji ufumu wace? popeza munena kuti nditurutsa ziwanda ndi Beelzebule.

19. Koma ngati Ine ndimaturutsa ziwanda ndi Beelzebule, ana anu aziturutsa ndi yani? Mwa ici iwo adzakhala oweruza anu.

20. Koma ngati Ine nditurutsa ziwanda ndi cala ca Mulungu, pamenepo Ufumu wa Mulungu wafikira inu.

21. Pamene pali ponse mwini mphamvu alonda pabwalo pace zinthu zace ziri mumtendere;

22. koma pamene pali ponse amdzera wakumposa mphamvu, nakamlaka, amcotsera zida zace zonse zimene anazitama, nagawa zofunkha zace.

23. Iye wosabvomerezana ndi Ine atsutsana ndi Ine; ndipo iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwaza.

24. Pamene pali ponse mzimu wonyansa ukaturuka mwa munthu, upyola malo opanda madzi nufunafuna mpumulo; ndipo posaupeza unena, Ndidzabwera kunyumba kwanga kumene ndinaturukako;

25. ndipo pofika, uipeza yosesa ndi yokonzeka.

26. Pomwepo, upita nutenga mizimu yina isanu ndi iwiri yoipa yoposa ndi uwu mwini; ndipo ilowa nikhalira komweko; ndipo makhalidwe otsiriza a munthu uyu aipa koposa oyambawo.

Werengani mutu wathunthu Luka 11