Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 10:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zitatha izi Ambuye anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiri awiri pamaso pace ku mudzi uli wonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini.

2. Ndipo ananena kwa iwo, Dzinthu dzicuruka, koma anchito acepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe anchito kukututa kwace.

3. Mukani; taonani, Ine ndituma inu ngati ana a nkhosa pakati pa mimbulu.

4. Musanyamule thumba la ndalama kapena thumba la kamba, kapena nsapato; nimusalankhule munthu panjira.

5. Ndipo m'nyumba iri yonse mukalowamo muthange mwanena, Mtendere ukhale pa nyumba iyi.

6. Ndipo mukakhala mwana wa mtendere m'menemo, mtendere wanu udzapumula pa iye; koma ngati mulibe, udzabwerera kwa inu.

7. Ndipo m'nyumba momwemo khalani, ndi kudya ndi kumwa za kwao; pakuti wanchito ayenera mphotho yace; musacokacoka m'nyumba.

8. Ndipo m'mudzi uli wonse mukalowamo, ndipo alandira inu, idyani zomwezi akupatsani;

9. ndipo ciritsani odwala ali mamwemonimunene nao, Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu. Koma ku mudzi uli wonse mukalowako,

10. ndipo salandira inu, m'mene mwaturuka ku makwalala ace nenani,

11. Lingakhale pfumbi locokera kumudzi kwanu, lomamatika ku mapaziathu, tilisansira pa inu; koma zindikirani ici, kuti Ufumu wa Mulungu wayandikira.

Werengani mutu wathunthu Luka 10