Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 1:1-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. POPEZA ambiri anayesa kulongosola nkhani ya zinthu zinacitika pakati pa ife,

2. monga anazipereka kwa ife iwo amene anakhala mboni ndi atumiki a mau,

3. kuyambira paciyambi, ndinayesa nkokoma inenso, amene ndinalondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira paciyambi, kulembera kwa iwe tsatane tsatane, Teofilo wabwinotu iwe;

4. kuti udziwitse zoona zace za mau amene unaphunzira.

5. Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lace Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wace wa ana akazi a pfuko la Aroni, dzina lace Elisabeti.

6. Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osacimwa.

7. Ndipo analibe mwana, popeza Elisabeti anali wouma, ndipo onse awiri anakalamba.

8. Ndipo panali, pakucita iye nchito yakupereka nsembe m'dongosolo la gulu lace, pamaso pa Mulungu, monga mwa macitidwe a kupereka nsembe,

9. adamgwera maere akufukiza zonunkhira polowa iye m'Kacisi wa Ambuye.

10. Ndipo khamu lonse la anthu Iinalikupemphera kunja nthawi ya zonunkhira.

11. Ndipo anamuonekera iye mngelo wa Ambuye, naimirira ku dzanja lamanja la guwa la nsembe la zonunkhira.

12. Ndipo Zakariya anadabwa pamene anamuona, ndipo mantha anamgwira.

13. Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zakariya, cifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamucha dzina lace Yohane.

14. Ndipo udzakhala nako kukondwera ndi msangalalo; ndipo anthu ambiri adzakondwera pa kubadwa kwace.

15. Pakuti iye adzakhala wamkuru pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena, kacasu; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asanabadwe.

16. Ndipo iye adzatembenuzira ana a Israyeli ambiri kwa Ambuye Mulungu wao.

17. Ndipo adzamtsogolera iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.

Werengani mutu wathunthu Luka 1