Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 9:3-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo m'utsimo mudaturuka dzombe padziko, ndipo analipatsa ilo mphamvu monga zinkhanira za dziko ziri ndi mphamvu.

4. Ndipo ananena kwa ilo kuti lisaipse udzu wa padziko, kapena cabiriwiri ciri conse, kapena mtengo uli wonse, koma anthu amene alibe cizindikilo ca Mulungu pamphumi pao ndiwo.

5. Ndipo anapatsa ilo mphamvu si kuti likawaphe, komatu kuti likawazunze miyezi isanu; ndipo mazunzidwe ao anali ngati mazunzidwe a cinkhanira, pamene ciluma munthu.

6. Ndipo m'masiku ajawo, anthu adzafunafuna imfa osaipeza konse; ndipo adzakhumba kumwalira, koma imfa idzawathawa.

7. Ndipo maonekedwe a dzombelo anafanana ndi akavalo okonzeka kukacita nkhondo; ndi pamitu pao ngati akorona onga agolidi, ndi pankhope pao ngati pankhope pa anthu.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 9