Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 9:3-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo m'utsimo mudaturuka dzombe padziko, ndipo analipatsa ilo mphamvu monga zinkhanira za dziko ziri ndi mphamvu.

4. Ndipo ananena kwa ilo kuti lisaipse udzu wa padziko, kapena cabiriwiri ciri conse, kapena mtengo uli wonse, koma anthu amene alibe cizindikilo ca Mulungu pamphumi pao ndiwo.

5. Ndipo anapatsa ilo mphamvu si kuti likawaphe, komatu kuti likawazunze miyezi isanu; ndipo mazunzidwe ao anali ngati mazunzidwe a cinkhanira, pamene ciluma munthu.

6. Ndipo m'masiku ajawo, anthu adzafunafuna imfa osaipeza konse; ndipo adzakhumba kumwalira, koma imfa idzawathawa.

7. Ndipo maonekedwe a dzombelo anafanana ndi akavalo okonzeka kukacita nkhondo; ndi pamitu pao ngati akorona onga agolidi, ndi pankhope pao ngati pankhope pa anthu.

8. Ndipo anali nalo tsitsi Ionga tsitsi la akazi, ndipo mano ao analingati mano a mikango.

9. Ndipo anali nazo zikopa ngati zikopa zacitsulo; ndipo mkokomo wa: mapiko ao ngati mkokomo wa agareta, a akavalo ambiri akuthamangira kunkhondo.

10. Ndipo liri nayo micira yofanana ndi ya cinkhanira ndi mbola; ndipo m'micira mwao muli mphamvu yao yakuipsa anthu miyezi isanu.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 9