1. Ndipo mngelo wacisanu anaomba, ndipo ndinaona nyenyezi yocokera kumwamba idagwa padziko; ndipo anampatsa iye cifunguliro ca dzenje la phompho.
2. Ndipo anatsegula pa dzenje la phompho; ndipo unakwera utsi woturuka m'dzenjemo, ngati utsi wa ng'anjo yaikuru; ndipo dzuwa ndi thambo zinada, cifukwa ca utsiwo wa kudzenje,
3. Ndipo m'utsimo mudaturuka dzombe padziko, ndipo analipatsa ilo mphamvu monga zinkhanira za dziko ziri ndi mphamvu.