Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 7:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zitatha izi ndinao na angelo anai alinkuimirira pa ngondya zinai za dziko, akugwira mphepo zinai za dziko, kuti ingaombe mphepo padziko, kapena panyanja, kapena pa mtengo uli wonse.

2. Ndipo ndinaona mngelo wina, anakwera kucokera poturuka dzuwa, ali naco cizindikilo ca Mulungu wamoyo: ndipo anapfuula ndi mau akuru kuitana angelo anai, amene adalandira mphamvu kuipsa dziko ndi nyanja,

3. nanena, Musaipse dziko, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira tidasindikiza cizindikilo akapolo a Mulungu wathu, pamphumi pao.

4. Ndipo ndinamva ciwerengo ca iwo osindikizidwa cizindikilo, zikwi makumi khumi ndi makumi anai mphambu anai, osindikizidwa cizindikilo mwa mafuko onse a ana a Israyeli,

5. Mwa pfuko la Yuda anasindikizidwa cizindikilo zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Rubeni zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Gadi zikwi khumi ndi ziwiri:

6. Mwa pfuko la Aseri zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Nafitali zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Manase zikwi khumi ndi ziwiri:

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 7