Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 5:4-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo ndinalira kwambiri, cifukwa sanapezedwa mmodzi woyenera kutsegula bukulo, kapena kulipenya;

5. ndipo mmodzi wa akuru ananena ndi ine, Usalire: taona, Mkango wocokera m'pfuko la Yuda, Muzu wa Davide, walakika kutsegula buku ndi zizindikilo zace zisanu ndi ziwiri.

6. Ndipo ndinaona pakati pa mpando wacifumu ndi zamoyo zinai, ndi pakati pa akuru, Mwanawankhosa ali ciriri ngati waphedwa; wokhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri, ndi maso asanu ndi awiri, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, yotumidwa ilowe m'dziko lonse.

7. Ndipo anadza, nalitenga ku dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wacifumu.

8. Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse ziri nao azeze, ndi mbale zagolidi zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.

9. Ndipo ayimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikilo zace; cifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 5