Ndipo ndinaona pakati pa mpando wacifumu ndi zamoyo zinai, ndi pakati pa akuru, Mwanawankhosa ali ciriri ngati waphedwa; wokhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri, ndi maso asanu ndi awiri, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, yotumidwa ilowe m'dziko lonse.