Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 4:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zitatha izi ndinapenya, ndipo taonani, khomo lotseguka m'Mwamba, ndipo mau oyamba ndinawamva, ngati lipenga Iakulankhuia ndi ine, anati, Kwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene ziyenera kucitika m'tsogolomo.

2. Pomwepo ndinakhala mwa Mzimu; ndipo, taonani padaikika mpando wacifumu m'Mwamba ndi pa mpandowo padakhala wina;

3. ndipo maonekedwe a iye wokhalapo anafanana ndi mwaia wa jaspi, ndi sardiyo; ndipo panali utawaleza wozinga mpando wacifumu, maonekedwe ace ngati smaragido.

4. Ndipo pozinga mpando yacifumu mipando yacifumu makumi awiri mphambu inai; ndipo pa mipandoyo padakhala akuru makumi awiri mphambu anai, atabvala zobvala zoyera, ndi pamitu pao akorona agolidi.

5. Ndipo mu mpando wacifumu mudaturuka mphezi ndi mau ndi mabingu. Ndipo panali nyali zisanu ndi ziwiri za mota zoyaka ku mpando wacifumu, ndiyo Mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu;

6. ndipo ku mpandowo, ngati nyanja, yamandala yonga krustalo; ndipopakati pa mpandowo, ndi pozinga mpandowo, zamoyo zinai zodzaia ndi maso kutsogolo indi kumbuyo.

7. Ndipo camoyo coyamba cinafanana nao mkango, ndi camoyo caciwiri cinafanana ndi mwana wa ng'ombe, ndi camoyo cacitatu cinali nayo nkhope yace ngati ya munthu, ndi camoyo cacinai cidafanana ndi ciombankhanga cakuuluka.

8. Ndipo zamoyozo zinai, conse pa cokha cinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m'katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 4