Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 21:17-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo anayesa linga lace, mikono zana mphambu makumi anai kudza zinai, muyeso wa munthu, ndiye mngelo.

18. Ndipo mirimo ya linga lace ndi yaspi; ndipo mzindawo ngwagolidi woyengeka, wofanana ndi mandala oyera.

19. Maziko a linga la mzinda anakometsedwa ndi miyala ya mtengo, ya mitundu mitundu; mazikooyamba, ndi yaspi; aciwiri, ndi safiro; acitatu, ndi kalikedo; acinai, ndi smaragido;

20. acisanu, ndi sardoau; acisanu ndi cimodzi, ndi sardiyo; acisanu ndi ciwiri, ndi krusolito; acisanu ndi citatu, ndi berulo; acisanu ndi cinai, ndi topaziyo; akhumi, ndi krusoprazo; akhumi ndt cimodzi, ndi huakinto; akhumi ndi ciwiri, ndi ametusto.

21. Ndipo zitseko khumi ndi ziwiri ndizo ngale khumi ndi ziwiri; citseko ciri conse pa cokha ca ngale imodzi. Ndipo khwalala la mzinda ma golidi woyengeka, ngati mandala openyekera.

22. Ndipo siridinaona Kacisi momwemo; pakuti Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, ndi Mwanawankhosa ndiwo Kacisi wace.

23. Ndipo 1 pamzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uunikira umenewu, ndipo nyali yace ndiye Mwanawankhosa.

24. Ndipo 2 amitundu adzayendayenda mwa kuunika kwace; ndi mafumu a dziko atenga ulemerero wao kulowa nao momwemo.

25. Ndipo 3 pa zipata zace sipatsekedwa konse usana, 4 (pakuti sikudzakhala usiku komweko);

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 21