Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 2:6-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Koma ici uli naco, kuti udana nazo nchito za Anikalai, zimene Inenso ndidana nazo.

7. Iye wokhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo, K wa iye amene alakika ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli m'Paradaiso wa Mulungu.

8. Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Smurna lemba;Izi anena woyamba ndi wotsiriza, amene anakhala wakufa, nakhalanso ndi moyo:

9. Ndidziwa cisautso cako, ndi umphawi wako (komatu uli wacuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana.

10. Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena ainu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala naco cisautso masiku khumi. Khala wokholupirfka kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.

11. Iye wokhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene alakika sadzacitidwa coipa ndi imfa yaciwiri.

12. Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Pergamo lemba:Izi anena iye wokhala nalo lupanga lakuthwa konse konse:

13. Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wacifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza cikhulupiriro canga, angakhale m'masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.

14. Komatu ndiri nazo zinthu pang'ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nao komweko akugwira ciphunzitso ca Balamu, amene anaphunzitsa Balaki aponye cokhumudwitsa pamaso pa ana a Israyeli, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, nacite cigololo.

15. Kotero uli nao akugwira ciphunzitso ca Anikolai momwemonso.

16. Cifukwa cace lapa; ukapanda kutero ndidza kwa iwe posacedwa, ndipo ndidzacita nao nkhondo ndi lupanga la m'kamwa mwanga.

17. Iye wakukhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wolakika, ndidzampatsa mana obisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pa mwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu ali yense koma iye wakuulandira.

18. Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Tiyatira lemba:Izi azinena Mwana wa Mulungu, wakukhala nao maso ace ngati lawi la moto, ndi mapazi ace ngati mkuwa wonyezimira:

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 2