Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 19:9-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo ananena ndi ine, Lemba, Odala iwo amene aitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo ananena ndi ine, Iwo ndiwo mau oona a Mulungu.

10. Ndipo ndinagwa pa mapazi ace kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa cinenero.

11. Ndipo ndinaona mutatseguka m'Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi iye wakumkwera wochedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nacita nkhondo molungama.

12. Ndipo maso ace ali lawi la moto, ndi pamutu pace pali nduwira zacifumu zambiri; ndipo ali nalo dzina lolembedwa, wosalidziwa wina yense koma iye yekha.

13. Ndipo abvala cobvala cowazidwa mwazi; ndipo achedwa dzina lace, Mau a Mulungu.

14. Ndipo magulu a nkhondo okhala m'Mwamba anamtsata iye, okwera pa akavalo oyera, obvala bafuta woyera woti mbu.

15. Ndipo m'kamwa mwace muturuka Iupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo iye adzawalamulira ndi ndodo yacitsulo: ndipo aponda iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 19