Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 14:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo alikuimirira pa phiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi iye zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, akukhala nalo dzina lace ndi dzina la Atate wace lolembedwa pamphumi pao.

2. Ndipo ndinamva mau ocokera Kumwamba, ngati mkokomo wamadzi ambiri, ndi ngati mau a bingu lalikuru; ndipo mauamene ndinawamva anakhala ngati a azeze akuyimba azeze ao j

3. ndipo ayimba ngati nyimbo yatsopane ku mpando wacifumu, ndi pamaso pa zamoyo zinai, ndi akulu; ndipo palibe munthu anakhoza kuphunzira nyimboyi, kama zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, ogulidwa kucokera kudziko.

4. Iwo ndiwo amene sadetsedwa pamodzi ndi akazi; pakuti ali anamwali. Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kulikonse amukako. Iwowa anagulidwa mwa anthu, zipatso zoundukulakwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.

5. Ndipo m'kamwa mwao simunapezedwa bodza; ali opanda cirema.

6. Ndipo ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nao Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uti wonse ndi pfuko ndi manenedwe ndi anthu j

7. ndi kunena ndi mau akuru, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya ciweruziro cace; ndipo mlambireni iye amene analenga m'mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi,

8. Ndipo anatsata mngelo wina mnzace ndi kunena, Wagwa, wagwa, Babulo waukuru umene unamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa cigololo cace.

9. Ndipo anawatsata mngelo wina, wacitatu, nanena ndi mau akuru, Ngati wina alambira ciromboco, ndi fane lace, nalandira lembapamphumi pace, kapena pa dzanja lace,

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 14