Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 13:13-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo cicita zizindikilo zazikuru, kutinso citsitse moto ucokere m'mwamba nugwe padziko, pamaso pa anthu.

14. Ndipo cisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikilo zimene anacipatsa mphamvu yakuzicita pamaso pa cirombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fane la ciromboco, cimene cinali nalo bala la lupanga nicinakhalanso ndi moyo.

15. Ndipo anacipatsa mphamvu yakupatsa fano la cirombo mpweya, kutinso fane la cirombo Iilankhule, nilicite kuti onse osalilambira fane la cirombo aphedwe.

16. Ndipo cicita kuti onse, ang'ono ndi akuru, acuma ndi osauka, ndi mfulu ndi akapolo, alandire cilembo pa dzanja lao ndi pamphumi pao;

17. ndi kuti munthu sangakhoze kugula kapena kugulitsa, koma iye yekha wakukhala naco cilembo, ndilo dzina la cirombo, kapena ciwerengero ca dzina lace.

18. Pano pali nzeru. Iye wakukhala naco cidziwitso awerenge ciwerengero ca ciromboco; pakuti ciwerengero cace ndi ca munthu; ndipo ciwerengero cace ndico mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi cimodzi.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 13